Judges 6:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina mngelo wa Chauta adabwera ku Ofura ndi kukhala pansi patsinde pa mtengo wa thundu umene unali wa Yoasi Mwabiyezere. Nthaŵiyo nkuti Gideoni, mwana wake, akupuntha tirigu, atabisala m'nyumba yofinyira mphesa, kuti Amidiyani asamuwone tiriguyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala m'Ofura, wa Yowasi Mwabiyezere; ndi mwana wake Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidiyani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina mngelo wa Yehova anabwera ku Ofura ndi kukhala pansi pa tsinde pa mtengo wa thundu umene unali wa Yowasi Mwabiezeri. Tsono Gideoni, mwana wake nʼkuti pa nthawiyo akupuntha tirigu mʼmalo ofinyira mphesa mowabisalira Amidiyani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala m'Ofira, wa Yoasi M-abieziri; ndi mwana wace Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidyani.