Judges 6:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gideoni adauza mngeloyo kuti, “Pepani mbuyanga, ngati Chauta ali nafe, chifukwa chiyani tsono zonsezi zatigwera? Nanga zili kuti ntchito zake zonse zodabwitsa zimene makolo athu ankatisimbira zakuti ati Chauta adatitulutsa ku dziko la Ejipito? Koma tsopano watitaya, ndipo watipereka kwa Amidiyani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Gideoni ananena naye, Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe chatigwera ife bwanji chonsechi? Ndipo zili kuti zodabwitsa zake zonse zimene makolo athu anatiwerengera, ndi kuti, Sanatikweze kodi Yehova kuchokera m'Ejipito? Koma tsopano Yehova watitaya natipereka m'dzanja la Midiyani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gideoni anayankha, “Koma mbuye wanga, ngati Yehova ali nafedi, nʼchifukwa chiyani zonsezi zationekera? Nanga ntchito zake zodabwitsa zimene makolo athu anatiwuza pamene anati, ‘Yehova anatitulutsa ku dziko la Igupto,’ zili kuti? Koma tsopano Yehova watitaya ndi kutipereka mʼmanja mwa Amidiyani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Gideoni ananena naye, Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe catigwera ife bwanji conseci? ndipo ziti kuti zodabwiza zace zonse zimene makolo athu anatiwerengera, ndi kuti, Sanatikweza kodi Yehova kucokera m'Aigupto? Koma tsopano Yehova watitaya natipereka m'dzanja la Midyani.