Judges 6:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Gideoni adayankha kuti, “Inu Chauta, ndapota nanu, kodi ndingathe bwanji kupulumutsa Aisraele? Onani, mbumba yanga ndiye yofooka kwambiri m'fuko la Manase, ndipo m'banja mwa bambo wanga, wamng'ono koposa ndine.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa Iye, Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israele ndi chiyani? Taonani, banja langa lili loluluka m'Manase, ndipo ine ndine wamng'ono m'nyumba ya atate wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Gideoni anafunsa kuti, “Kodi Ambuye anga ine ndingapulumutse bwanji Israeli? Mbumba yanga ndi yopanda mphamvu mu fuko la Manase, ndiponso ine ndine wamngʼono kwambiri mʼbanja mwa abambo anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iye, Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israyeli ndi ciani? Taonani, banja langa liri loluluka m'Manase, ndipo ine ndine wamng'ono m'nyumba ya atate wanga.