Judges 6:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musachoke pano, ndapota nanu, mpaka nditabwerera kwa inu kudzakutulirani chopereka cha chakudya.” Apo Chauta adati, “Chabwino, ndikudikira mpaka utabwerera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musachoke pano, ndikupemphani, mpaka ndikudzerani ndi kutulutsa chopereka changa ndi kuchiika pamaso panu. Ndipo anati, Ndidzalinda mpaka ubwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chonde musachoke msanga mpaka nditabwerera kwa inu ndi chopereka changa cha chakudya kudzachipereka kwa inu.” Ndipo Yehova anamuwuza kuti, “Ine ndikudikira mpaka utabweranso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musacoke pano, ndikupemphani, mpaka ndikudzerani ndi kuturutsa copereka canga ndi kuciika pamaso panu. Ndipo anati, Ndidzalinda mpaka ubwera.