Judges 6:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Gideoni adakaloŵa m'nyumba mwake, nakakonza mwanawambuzi, naphika makeke osatupitsa a ufa wa makilogramu khumi. Nyamayo adaiika m'dengu ndipo msuzi wake adauthira mu mphika, nabwera nazo zonsezo kudzazipereka kwa mngelo uja patsinde pa mtengo wa thundu paja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda chotupitsa ya efa wa ufa; nyamayi anaiika m'lichero, ndi msuzi anauthira mumbale, natuluka nazo kwa Iye ali patsinde pa thundu, nazipereka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gideoni analowa mʼnyumba, ndipo anakakonza mwana wambuzi, nakonzanso makeke wopanda yisiti a ufa wa makilogalamu khumi. Nayika nyamayo mʼdengu ndipo msuzi wake anawuthira mu mʼphika. Anabwera nazo ndi kukazipereka kwa mngelo uja pa tsinde pa mtengo wa thundu paja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda cotupitsa ya muyeso wa ufa; nyamayi anaiika m'licero, ndi msuzi anauthira mumbale, naturuka nazo kwa iye ali patsinde pa thundu, nazipereka.