Judges 6:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amidiyani anali amphamvu ndi oopsa kupambana Aisraele. Nchifukwa chake Aisraele ankakumba malo obisalamo m'mapiri ndiponso m'mapanga, namanganso malinga ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene dzanja la Midiyani linalaka Israele, ana a Israele anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga chifukwa cha Midiyani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amidiyani anapondereza Aisraeli. Tsono chifukwa cha Amidiyaniwa, Aisraeli anakonza malo obisalamo mʼmapiri ndi mʼmapanga. Anamanganso malinga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene dzanja la Midyani linalaka Israyeli, ana a Israyeli anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga cifukwa ca Midyani.