Judges 6:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mngelo wa Chauta adatenga ndodo m'manja mwake nakhudza nayo nyama ija ndi makeke aja. Pompo padabuka moto pathanthwepo ndi kupsereza nyamayo pamodzi ndi makeke aja. Basi mngelo wa Chauta adazimirira osaonekanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lake, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo unatuluka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda chotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wa Yehova anatenga msonga ya ndodo imene inali mʼmanja mwake nakhudza nayo nyama ndi makeke aja. Nthawi yomweyo moto unabuka pa thanthwepo ndi kupsereza nyama yonse ndi makeke aja. Ndipo mngelo wa Yehova sanaonekenso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lace, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda cotupitsa; ndipo unaturuka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda cotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pace.