Judges 6:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka pamwamba pa linga pano umange ndi miyala yoyala bwino guwa la Chauta, Mulungu wako. Tsono utenge ng'ombe yamphongo yachiŵiri ija ndi kuipereka kuti ikhale nsembe yopsereza, pogwiritsa ntchito mtengo wa fano la Asera limene udule ngati nkhunilo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng'ombe yachiwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zake uyese chifanizo walikhacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka umangire Yehova Mulungu wako guwa lansembe ndi miyala yoyala bwino pamwamba pa chiwunda chimenecho. Utenge ngʼombe ya mphongo yachiwiri ija ndipo uyipereke ngati nsembe yopsereza pogwiritsa ntchito mitengo ya fano la Asera imene udule ngati nkhunizo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng'ombe yaciwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zace uyese cifanizo walikhaco.