Judges 6:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene anthu am'mudzimo adadzuka m'mamaŵa, adangoona guwa la Baala litagwetsedwa, fano la Asera limene linali pambali pake litadulidwa, ndipo ng'ombe yamphongo yachiŵiri ija itaperekedwa nsembe pa guwa adaamangalo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuuka mamawa amuna akumudziwo, taonani, guwa la nsembe la Baala litagamuka, ndi chifanizo chinali pomwepo chitalikhidwa ndi ng'ombe yachiwiri yoperekedwa pa guwa la nsembe adalimanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a mu mzindamo atadzuka mʼmamawa anangoona guwa la Baala litagwetsedwa ndi fano la Asera limene linali pamwamba pake litadulidwa ndiponso ngʼombe yamphongo yachiwiri ija itaperekedwa ngati nsembe yopsereza pa guwa limene linamangidwa lija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuuka mamawa amuna a ku mudziwo, taonani, guwa la nsembe la Baala litagamuka, ndi cifanizo cinali pomwepo citalikhidwa ndi ng'ombe yaciwiri yoperekedwa pa guwa la nsembe adalimanga.