Judges 6:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye adayamba kufunsana kuti, “Wachita zimenezi ndani?” Atafufuza ndi kufunsafunsa, adati, “Gideoni, mwana wa Yoasi, ndiye amene wachita zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanenana wina ndi mnzake, Wachita ichi ndani? Ndipo atafunafuna nafunsafunsa, anati, Gideoni, mwana wa Yowasi wachita ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anafunsana wina ndi mnzake, “Wachita zimenezi ndani?” Atafufuza ndi kufunsafunsa, analingalira kuti, “Gideoni mwana wa Yowasi ndiye wachita zimenezi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanenana wina ndi mnzace, Wacita ici ndani? Ndipo atafunafuna nafunsafunsa, anati, Gideoni, mwana wa Yoasi wacita ici.