Judges 6:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo anthu am'mudzimo adauza Yoasi kuti, “Mutulutse mwana wako. Ayenera kufa popeza kuti wagwetsa guwa la Baala, ndipo wadula fano la Asera limene linali pambali pake pa guwalo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo amuna akumudziwo anati kwa Yowasi, Umtulutse mwana wako kuti afe; pakuti anagamula guwa la nsembe la Baala, pakutinso analikha chifanizo chinali pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anthuwo anawuza Yowasi kuti, “Tulutsa mwana wako, ayenera kufa chifukwa wagumula guwa lansembe la Baala ndipo wadula fano la Asera lomwe linali pamwamba pake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo amuna a ku mudziwo anati kwa Yoasi, Umturutse mwana wako kuti afe; pakuti anagamula guwa la nsembe la Baala, pakutinso analikha cifanizo cinali pomwepo.