Judges 6:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma onse amene adamuukirawo, Yoasi adaŵauza kuti, “Kodi inu ndinu amene mukuti mummenyere nkhondo Baala? Kodi ndinu amene mukuti mumtchinjirize? Aliyense amene amenyere Baala nkhondo, aphedwa maŵa m'maŵa. Ngati iye ndi mulungudi, adzimenyere nkhondo yekha, popeza kuti guwa lake lagwetsedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yowasi anati kwa onse akumuimirira, Kodi inu mumnenera Baala mlandu? Kapena kodi mudzampulumutsa iye? Iye amene amnenera mlandu aphedwe kukali m'mawa; akakhala mulungu adzinenere yekha mlandu, popeza wina wamgamulira guwa lake la nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yowasi anawuza anthu amene anamuzungulirawo kuti, “Kodi inu mukuti mukhale woyankhulira Baala mlandu? Kodi ndinu amene mukuti mumupulumutse? Amene akufuna kumumenyera nkhondo Baala akhala atafa pofika mmawa! Ngati Baalayo ndi mulungudi, musiyeni adzimenyere yekha nkhondo popeza munthu wina wamugwetsera guwa lansembe lake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yoasi anati kwa onse akumuimirira, Kodi inu mumnenera Baala mlandu? Kapena kodi mudzampulumutsa iye? iye amene amnenera mlandu aphedwe kukali m'mawa; akakhala mulungu adzinenere yekha mlandu, popeza wina wamgamulira guwa lace la nsembe.