Judges 6:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Mzimu wa Chauta udaloŵa mwa Gideoni. Choncho Gideoniyo adaimba lipenga, ndipo Aabiyezere aja adaitanidwa kuti amtsate.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mzimu wa Yehova unavala Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abiyezere analalikidwa kumtsata iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mzimu wa Yehova unatsikira pa Gideoni, ndipo anayimba lipenga kuyitana Abiezeri kuti amutsatire iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mzimu wa Yehova unabvana Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abieziri analalikidwa kumtsata iye.