Judges 6:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatuma amithenga m'dziko lonse la Manase, nawonso Amanasewo adaitanidwa kuti amtsate. Adatumanso amithenga kwa Aasere, Azebuloni ndiponso Anafutali. Onsewo adapita kukaŵachingamira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuma mithenga kwa Manase konse; ndi iwonso analalikidwa kumtsata iye; natuma mithenga kwa Asere, ndi kwa Zebuloni, ndi kwa Nafutali; iwo nadzakomana nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Manase kuti akamenye nkhondo ndipo Amanase anayitanidwanso kuti amutsate. Anatumanso amithenga kwa Aseri, Azebuloni ndi Anafutali, ndipo onsewo anapita kukakumana naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatuma mithenga kwa Manase konse; ndi iwonso analalikidwa kumtsata iye; natuma mithenga kwa Aseri, ndi kwa Zebuloni, ndi kwa Nafitali; iwo nadzakomana nao.