Judges 6:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
chabwino, tsono ine ndikuyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Mame akangogwa pa ubweya wankhosa pokhapo, koma panthaka nkukhala pouma, apo ndidziŵa kuti Inu mudzapulumutsadi Aisraele kudzera mwa ine, monga momwe mudanenera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
taonani, ndidzaika chikopa cha ubweya popunthira tirigu; pakakhala mame pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pouma, pamenepo ndidzadziwa kuti mudzapulumutsa Israele ndi dzanja langa monga mwanena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
onani, ine ndiyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Ngati mame adzagwera pa ubweya wankhosa pokhapa, pa nthaka ponse pakhala powuma, ndiye ndidziwa kuti mudzapulumutsadi Israeli ndi dzanja langa monga mwanenera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
taonani, ndidzaika cikopa ca ubweya popunthira tirigu; pakakhala mame pacikopa pokha, ndi panthaka ponse pouma, pamenepo ndidzadziwa kuti mudzapulumutsa Israyeli ndi dzanja langa monga mwanena.