Judges 6:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Gideoni adalankhulanso ndi Mulungu nati, “Musandipsere mtima, mundilole ndilankhulenso kamodzi kokhaka. Ndapota nanu, mulole kuti paubweya pokhapa pakhale pouma koma panthaka ponsepa pagwe mame.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Gideoni ananena ndi Mulungu, Mkwiyo wanu usandiyakire, ndinene kamodzi kokha: ndikuyeseni kamodzi kokha ndi chikopa; paume pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pakhale mame.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Gideoni anati kwa Mulungu, “Musandikwiyire. Mundilole ndiyankhule kamodzi kokhaka. Ndiyeseko kamodzi kokha ndi ubweyawu kuti pa ubweya pokhapa pakhale powuma koma pa nthaka ponse pakhale ponyowa ndi mame.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Gideoni ananena ndi Mulungu, Mkwiyo wanu usandiyakire, ndinene kamodzi kokha: ndikuyeseni kamodzi kokha ndi cikopa; paume pacikopa pokha, ndi panthaka ponse pakhale mame.