Judges 6:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankamanga zithando zao moyang'anana ndi Aisraele, ndi kuwononga zokolola zao zonse mpaka ku Gaza, osaŵasiyirako Aisraelewo chakudya chilichonse, nkhosa, ng'ombe kapenanso bulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nawamangira misasa, namaononga zipatso za m'dziko mpaka ufika ku Gaza, osawasiyira chochirira njala m'Israele, ngakhale nkhosa, kapena ng'ombe, kapena bulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anamanga misasa mʼdzikomo ndi kuwononga zokolola zawo zonse mpaka ku Gaza, ndipo sanawasiyireko chamoyo chilichonse Aisraeliwo, kaya nkhosa kapena ngʼombe ndi bulu yemwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nawamangira misasa, namaononga zipatso za m'dziko mpaka ufika ku Gaza, osawasiyira cocirira njala m'Israyeli, ngakhale nkhosa, kapena ng'ombe, kapena buru.