Judges 6:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo Amidiyani ankabwera ndi ng'ombe zao zomwe pamodzi ndi mahema ao. Ankabwera ambiri ngati dzombe. Kunali kosatheka kuŵaŵerenga anthuwo ndi ngamira zao. Ankaononga dzikolo pamene ankabwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anakwera nazo zoweta zao ndi mahema ao, analowa ngati dzombe kuchuluka kwao; iwowa ndi ngamira zao zomwe nzosawerengeka; ndipo analowa m'dziko kuliononga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo ankabwera ndi zoweta zawo ndi matenti awo omwe. Ankabwera ambiri ngati dzombe, motero kuti kunali kovuta kuwawerenga anthuwo ndi ngamira zawo. Tsono iwo ankabwera ndi kuwononga dziko lonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anakwera nazo zoweta zao ndi mahema ao, analowa ngati dzombe kucuruka kwao; iwowa ndi ngamila zao zomwe nzosawerengeka; ndipo analowa m'dziko kuliononga.