Judges 6:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chautayo adaŵatumizira mneneri. Ndipo iye adaŵauza kuti, “Zimene Chauta, Mulungu wa Israele, wanena ndi izi, ‘Ndine amene ndidakutsogolerani kuchokera ku Ejipito, nkukutulutsani m'dziko laukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israele, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ine ndinakukwezani kuchokera m'Ejipito, ndi kukutulutsani m'nyumba ya ukapolo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawatumizira mneneri amene anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndine amene ndinakutsogolerani kuchokera ku Igupto. Ndinakutulutsani mʼdziko la ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israyeli, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ine ndinakukwezani kucokera m'Aigupto, ndi kukuturutsani m'nyumba ya ukapolo;