Judges 7:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Yerubaala (ndiye kuti Gideoni) ndi anthu onse amene anali naye, adadzuka m'mamaŵa nakamanga zithando zankhondo pambali pa kasupe wa ku Harodi. Zithando za Amidiyani zinali m'chigwa kumpoto kwao, pafupi ndi phiri la More.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa chitsime cha Harodi, ndi misasa ya Midiyani inali kumpoto kwao, pa phiri la More m'chigwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeru-Baala (Gideoni) ndi anthu ake onse anadzuka mʼmamawa nakamanga misasa pambali pa kasupe ku Harodi. Misasa ya Amidiyani inali mʼchigwa kumpoto kwa phiri la More.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa citsime ca Harodi, ndi misasa ya Midyani inali kumpoto kwao, pa phiri la More m'cigwa.