Judges 7:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amidiyani ndi Aamaleke ndi anthu akuvuma adaaphimba chigwa chonse ngati dzombe chifukwa cha kuchuluka kwao. Ndipo ngamira zao zinali zosaŵerengeka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Amidiyani ndi Aamaleke ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'chigwa, kuchuluka kwao ngati dzombe; ndi ngamira zao zosawerengeka, kuchuluka kwao ngati mchenga wa m'mphepete mwa nyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amidiyani, Aamaleki ndi anthu ena onse akummawa anadzaza chigwa chonse ngati dzombe. Ngamira zawo zinali zambiri zosawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Amidyani ndi Aamaleki ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'cigwa, kucuruka kwao ngati dzombe; ndi ngamila zao zosawerengeka, kucuruka kwao ngati mcenga wa m'mphepete mwa nyanja.