Judges 7:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atafika pafupi, Gideoni adamva munthu akufotokozera mnzake maloto ake. Ankati, “Ine ndalota maloto. Ndinangoona mtanda wa buledi wabarele ukugubuduzika kutsikira ku zithando za Amidiyani ndipo unafika mpaka ku chithando china nuchigunda, kotero kuti chinagwa ndipo nkuphwasukaphwasuka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakufikako Gideoni, taonani, panali munthu analikufotokozera mnzake loto, nati, Taona, kulota ndinalota, ndipo tapenya, mtanda wa mkate wabarele unakunkhulirakunkhulira m'misasa ya Midiyani, nufika kuhema, numgunda nagwa, numpidigula kuti hema anakhala chigwere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gideoni atafika anangomva munthu wina akuwuza mnzake maloto ake kuti, “Ine ndinalota nditaona dengu la buledi wa barele likugubuduzika kupita ku misasa ya Amidiyani. Litafika linawomba tenti moti inagwa ndi kuphwasukaphwasuka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakufikako Gideoni, taonani, panali munthu analikufotokozera mnzace loto, nati, Taona, kulota ndinalota, ndipo tapenya, mtanda wa mkate wabarele unakunkhulira-kunkhulira m'misasa ya Midyani, nufika kuhema, numgunda nagwa, numpidigula kuti hema anakhala cigwere.