Judges 7:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mnzake uja adayankha kuti, “Zimenezi si kanthu kena koma nkhondo ya Gideoni, mwana wa Yoasi, munthu wa ku Israele. Mulungu wapereka Midiyani pamodzi ndi ankhondo ake onse m'manja mwake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mnzake anayankha nati, Ichi si china konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yowasi, munthu wa Israele; Mulungu wapereka Midiyani ndi a m'misasa onse m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mnzakeyo anamuyankha kuti, “Iyi ndi nkhondo ya Gideoni mwana wa Yowasi, wa ku Israeli. Mulungu wapereka Amidiyani pamodzi ndi ankhondo ake onse mʼdzanja mwake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mnzace anayankha nati, Ici si cina konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yoasi, munthu wa Israyeli; Mulungu wapereka Midyani ndi a m'misasa onse m'dzanja lace.