Judges 7:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gideoni atamva kufotokoza kwa malotowo pamodzi ndi kumasulira kwake, adagwada pansi nathokoza Mulungu, ndipo adabwerera ku zithando za Aisraele naŵauza kuti, “Dzukani, Chauta wapereka Amidiyani m'manja mwanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakumva Gideoni kufotokozera kwa lotolo ndi tanthauzo lake, anadziwerama; nabwera ku misasa ya Israele nati, Taukani, pakuti Yehova wapereka a m'misasa a Midiyani m'dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gideoni atamva za malotowo ndi kumasulira kwake, anapembedza Mulungu. Kenaka anabwerera ku msasa wa Israeli nawawuza kuti, “Dzukani popeza Yehova wapereka msasa wa Midiyani mʼmanja mwanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakumva Gideoni kufotokozera kwa lotolo ndi tanthauzo lace, anadziwerama; nabwera ku misasa ya Israyeli nati, Taukani, pakuti Yehova wapereka a m'misasa a Midyani m'dzanja lanu.