Judges 7:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵagaŵa anthu 300 aja m'magulu atatu, napereka malipenga ndi mbiya m'manja mwa onsewo, ndipo m'mbiyamo onse adaikamo nsakali zoyaka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anagawa amuna mazana atatu akhale magulu atatu, napatsa malipenga m'manja a iwo onse, ndi mbiya zopanda kanthu, ndi miuni m'kati mwa mbiyazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawagawa anthu 300 aja magulu atatu, nawapatsa malipenga mʼmanja mwawo ndi mbiya zimene mʼkati mwake munali nsakali zoyaka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anagawa amuna mazana atatu akhale magulu atatu, napatsa malipenga m'manja a iwo onse, ndi mbiya zopanda kanthu, ndi miuni m'kati mwa mbiyazo,