Judges 7:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adauza anthuwo kuti, “Muzindiyang'ana ine, ndipo muchite chimodzimodzi. Ndikafika ku malire a zithando, muchite zomwe ndichite ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena nao, Mundipenyerere ine, ndi kuchita momwemo; ndipo taonani, pakufika ine pa chilekezero cha misasa, kudzali, monga ndichita ine, momwemo muzichita inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawuza anthuwo kuti, “Muzikayangʼana ine ndi kuchita zimene ndizikachita. Ndikakafika kumalire a msasa, mukachite zomwe ndikachita ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena nao, Mundipenyerere ine, ndi kucita momwemo; ndipo taonani, pakufika ine pa cilekezero ca misasa, kudzali, monga ndicita ine, momwemo muzicita inu.