Judges 7:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikaimba lipenga, ineyo pamodzi ndi onse amene ali ndi ine, inunso muimbe malipenga ku mbali zonse za zithando zonse, ndipo mufuule kuti, ‘Lupanga la Chauta ndi la Gideoni.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene ndiomba lipenga, ine ndi onse okhala nane, inunso muziomba lipenga pozungulira ponse pa misasa, ndi kunena kuti, Yehova ndi Gideoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikadzaliza lipenga ndi onse amene ali ndi ine, inunso mukalize malipenga kumbali zonse za misasa yonse ndi kufuwula kuti, ‘Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene ndiomba lipenga, ine ndi onse okhala nane, inunso muziomba lipenga pozungulira ponse pa misasa, ndi kunena kuti, Yehova ndi Gideoni.