Judges 7:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Gideoni, pamodzi ndi anthu 100 amene anali naye aja, adafika ku malire a zithando pakati pa usiku, alonda atangosinthana chatsopano apa. Tsono adaimba malipenga, naswa mbiya zimene zinali m'manja mwao zija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku chilekezero cha misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m'manja mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Gideoni pamodzi ndi amuna 100 omwe anali nawo anafika ku malire a msasa pakati pa usiku, alonda atangosinthana kumene. Iwo analiza malipenga awo ndi kuphwanya mbiya zimene zinali mʼmanja mwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku cilekezero ca misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m'manja mwao.