Judges 7:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauza Gideoni kuti, “Anthu uli nawoŵa andichulukira kwambiri, kuti ndigonjetse Amidiyani, chifukwa Aisraele angamandipeputse Ine ndi kumanena kuti, ‘Tadzipulumutsa ndi mphamvu zathu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Gideoni. Anthu ali ndi iwe andichulukira kuti ndipereke Midiyani m'dzanja lao; angadzitame Israele pa Ine, ndi kuti, Dzanja la ine mwini landipulumutsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati kwa Gideoni, “Anthu uli nawowa andichulukira kwambiri kuti ndigonjetse Amidiyani chifukwa Aisraeli angamadzitukumule pamaso panga ndi kumanena kuti, ‘Tadzipulumutsa ndi mphamvu zathu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Gideoni. Anthu ali ndi iwe andicurukira kuti ndipereke Midyani m'dzanja lao; angadzitame Israyeli pa Ine, ndi kuti, Dzanja la ine mwini landipulumutsa.