Judges 7:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo magulu ena aŵiri aja nawonso adaimba malipenga, naswa mbiya zija, onse atatenga nsakali zija m'dzanja lakumanzere, ndi malipenga oti aziimba m'dzanja lamanja. Ndipo adafuula kuti, “Lupanga la Chauta ndi la Gideoni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi magulu atatuwo anaomba malipenga, naswa mbiyazo, nagwira miuni ndi dzanja lao lamanzere, ndi malipenga m'dzanja lao lamanja kuwaomba; ndipo anafuula, Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Magulu awiri ena aja anayimbanso malipenga ndi kuswa mbiya zawo. Aliyense ananyamula nsakali ya moto ku dzanja lamanzere ndi lipenga ku dzanja lamanja ndipo anafuwula kuti, “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi magulu atatuwo anaomba malipenga, naswa mbiyazo, nagwira miuni ndi dzanja lao lamanzere, ndi malipenga m'dzanja lao lamanja kuwaomba; ndipo anapfuula, Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.