Judges 7:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankhondo 300 aja a Gideoni ataimba malipenga, Chauta adamenyanitsa ankhondo aja a Midiyani. Onse adasokonezeka, mwakuti ankamenyana okhaokha. Ankhondowo adathaŵira ku Betesita cha ku Zerera, mpaka ku malire a Abele-Mehola pafupi ndi Tabati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mazana atatuwa anaomba malipenga, ndipo Yehova anakanthanitsa yense mnzake ndi lupanga m'misasa monse; ndi a m'misasa anathawa mpaka ku Betesita ku Zerera, mpaka ku malire a Abele-Mehola pa Tabati.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu 300 aja ataliza malipenga, Yehova anawasokoneza ankhondo a Midiyani aja motero kuti ankamenyana okhaokha. Ankhondowo anathawira ku Beti-Sita cha ku Zerera mpaka ku malire a Abeli-Mehola pafupi ndi Tabati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mazana atatuwa anaomba malipenga, ndipo Yehova anakanthanitsa yense mnzace ndi lupanga m'misasa monse; ndi a m'misasa anathawa mpaka ku Betesita ku Zerera, mpaka ku malire a Abelemehola pa Tabati.