Judges 7:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gideoni adatuma amithenga m'dziko lonse lamapiri la Efuremu kuti akanene kuti, “Tsikani mudzalimbane ndi Amidiyani, ndipo mulande madooko ao oolokera mpaka Betebara ndiponso mtsinje wa Yordani.” Choncho Aefuremu onse adasonkhana, nalanda madooko mpaka ku Betebara ndiponso mtsinje wa Yordani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Gideoni anatumanso mithenga ku mapiri onse a Efuremu ndi kuti, Tsikani, kukomana ndi Amidiyani ndi kutsekereza madooko asanafike iwowa, mpaka ku Betebara ndi Yordani. Potero amuna onse a Efuremu anasonkhana pamodzi natsekereza madooko mpaka ku Betebara, ndi Yordani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gideoni anatumiza amithenga ku dziko lonse la ku mapiri la Efereimu kukanena kuti, “Tsikani mumenyane ndi Amidiyani ndipo mulande madooko awo owolokera mpaka ku Beti-Bara.” Choncho anthu onse a fuko la Efereimu anasonkhana ndipo analanda madooko awo owolokera mpaka ku Betibaala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Gideoni anatumanso mithenga ku mapiri onse a Efraimu ndi kuti, Tsikani, kukomana ndi Amidyani ndi kutsekereza madooko asanafike iwowa, mpaka ku Beti-bara ndi Yordano. Potero amuna onse a Efraimu anasonkhana pamodzi natsekereza madooko mpaka ku Betibara, ndi Yordano.