Judges 7:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adagwira mafumu aŵiri a Midiyani, Orebu ndi Zebu. Adapha Orebu ku thanthwe la Orebu, ndipo Zebu adamuphera ku malo ofinyira mphesa ku Zebu, pamene ankapirikitsa Amidiyani. Tsono adabwera ndi mutu wa Orebu ndi wa Zebu kwa Gideoni kutsidya kwa Yordani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anagwira akalonga awiri a Midiyani, Orebu ndi Zeebu; namupha Orebu ku thanthwe la Orebu; ndi Zeebu anamupha ku choponderamo mphesa cha Zeebu, nalondola Amidiyani; ndipo anadza nayo mitu ya Orebu ndi Zeebu kwa Gideoni tsidya lija la Yordani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anagwiranso atsogoleri awiri a nkhondo a Amidiyani, Orebu ndi Zeebu. Anapha Orebu ku thanthwe la Orebu, koma Zeebu anamuphera ku malo ofinyira mphesa ku Zeebu pothamangitsa Amidiyani. Mitu ya Orebu ndi Zeebu anabwera nayo kwa Gideoni kutsidya kwa Yorodani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anagwira akalonga awiri a Midyani, Orebi ndi Zeebi; namupha Orebi ku thanthwe la Orebi; ndi Zeebi anamupha ku coponderamo mphesa ca Zeebi, nalondola Amidyani; ndipo anadza nayo mitu ya Orebi ndi Zeebi kwa Gideoni tsidya lija la Yordano.