Judges 7:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ulengeze kwa anthu kuti, ‘Aliyense amene akuchita mantha ndi kunjenjemera, abwerere kwao.’ ” Ndiye anthu okwanira 22,000 adabwerera, natsala 10,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, kalalike m'makutu a anthu, ndi kuti, Aliyense wochita mantha, nanjenjemera, abwerere nachoke pa phiri la Giliyadi. Ndipo anabwererako anthu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, natsalako zikwi khumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono lengeza kwa anthu kuti, ‘Aliyense amene akuchita mantha ndi kunjenjemera abwerere kwawo, ndipo achoke kuno ku phiri la Giliyadi.’ ” Choncho anthu 22,000 anachoka, ndipo anatsalira anthu 10,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, kalalike m'makutu a anthu, ndi kuti, Ali yense wocita mantha, nanjenjemera, abwerere nacoke pa phiri la Gileadi. Ndipo anabwererako anthu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, natsalako zikwi khumi.