Judges 7:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauzanso Gideoni kuti, “Anthuŵa akundichulukirabe kwambiri. Uŵatenge, upite nawo ku madzi, ndipo ndikaŵayesa ndine m'malo mwako kumeneko. Amene ndikuuze kuti, ‘Uyu apite nao,’ adzapita nao. Ndipo amene ndikuuze kuti, ‘Uyu asapite nao,’ sadzapita nao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova ananena ndi Gideoni, Anthu akali ochuluka; tsikira nao kumadzi, ndipo ndidzakuyesera iwo komweko; ndipo kudzali kuti iye amene ndimnena kwa iwe, Uyo azimuka nawe, yemweyo azimuka nawe; koma aliyense ndimnena kwa iwe, Uyo asamuke nawe, yemweyo asamuke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova anawuza Gideoni kuti, “Anthuwa achulukabe. Uwatenge upite nawo ku mtsinje ndipo ndikawayesa kumeneko mʼmalo mwako. Ndikadzanena kuti, ‘Uyu apite nawe’ adzapita nawe; koma ndikanena kuti ‘Uyu asapite nawe,’ sadzapita nawe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova ananena ndi Gideoni, Anthu akali ocuruka; tsikira nao kumadzi, ndipo ndidzakuyesera iwo komweko; ndipo kudzali kuti iye amene ndimnena kwa iwe, Uyo azimuka nawe, yemweyo azimuka nawe; koma ali yense ndimnena kwa iwe, Uyo asamuke nawe, yemweyo asamuke.