Judges 7:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Gideoni adapita nawo anthu aja kumadziko. Ndipo Chauta adamuuza kuti, “Onse amene akhathire madzi pakumwa ndi lilime, monga m'mene amachitira galu, uŵaike paokha. Ndipo onse amene agwade kuti amwe madzi, uŵaikenso paokha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Aliyense akapiza madzi pa lilime lake, monga akhatira galu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo aliyense agwada pakumwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Gideoni anatenga anthuwo ndi kupita nawo ku madzi. Kumeneko Yehova anamuwuza kuti, “Amene amwe madzi mokhathira ndi manja ngati galu uwayike pawokha, ndipo amene amwe atagwada pansi uwayikenso pawokha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ali yense akapiza madzi pa lilime lace, monga akhatira garu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo ali yense agwada pakumwa.