Judges 7:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Gideoni adatumiza onse kwao kupatula anthu 300 aja. Tsono osankhidwawo adatenga chakudya ndi malipenga a anthuwo. Zithando zankhondo za Amidiyani zinali chakumunsi m'chigwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israele amuke, yense kuhema kwake; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midiyani inali kunsi kwake m'chigwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho analola anthu ena onse kuti apite ku nyumba zawo kupatula anthu 300 osankhika aja. Iwowa anatenga zakudya ndi malipenga a anthuwo. Ndipo misasa ya ankhondo Amidiyani inali kumunsi kwa chigwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israyeli amuke, yense kuhema kwace; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midyani inali kunsi kwace m'cigwa.