Judges 8:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Aefuremu adamufunsa Gideoni kuti, “Kodi udalekeranji kutiitana ife pamene unkakamenyana ndi Amidiyani?” Ndipo adamkalipira kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amuna a Efuremu anati kwa iye, Ichi watichitira nchiyani, osatiitana popita iwe kulimbana ndi Amidiyani? Natsutsana naye kolimba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aefereimu anafunsa Gideoni kuti, “Nʼchifukwa chiyani watichita zimenezi? Bwanji sunatiyitane pamene umakamenyana ndi Amidiyani?” Iwo anamudzudzula kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amuna a Efraimu anati kwa iye, Ici waticitira nciani, osatiitana popita iwe kulimbana ndi Amidyani? natsutsana naye kolimba.