Judges 8:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵiyo nkuti Zeba ndi Zalimuna ali ku Karikori pamodzi ndi ankhondo ao, anthu pafupi 15,000. Iwoŵa ndiwo amene adatsalako mwa ankhondo a anthu akuvuma, pakuti ankhondo adaafapo 120,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zeba ndi Zalimuna ndipo anali m'Karikori, ndi a m'misasa ao pamodzi nao, amuna monga zikwi khumi ndi zisanu; ndiwo otsala onse a khamu lonse la ana a kum'mawa; popeza atagwa amuna zikwi zana limodzi ndi makumi awiri akusolola lupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi iyi nʼkuti Zeba ndi Zalimuna ali ku Karikori ndi ankhondo pafupifupi 15,000. Amenewa ndiwo anatsalako mwa ankhondo a anthu akummawa; pakuti anafa ankhondo 120,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zeba ndi Tsalimuna ndipo anali m'Karikori, ndi a m'misasa ao pamodzi nao, amuna monga zikwi khumi ndi zisanu; ndiwo otsala onse a khamu lonse la ana a kum'mawa; popeza atagwa amuna zikwi zana limodzi ndi makumi awiri akusolola lupanga.