Judges 8:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gideoni adadzera njira ya anthu okhala m'mahema kuvuma kwa Noba ndi Yogobeha, ndipo adaŵathira nkhondo ankhondowo, pakuti anali osakonzekera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Gideoni anakwerera njira ya iwo okhala m'mahema kum'mawa kwa Noba, ndi Yogobeha, nakantha khamulo popeza khamulo linakhala lokhazikika mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gideoni anadzera njira ya anthu a matenti kummawa kwa Noba ndi Yogibeha ndipo anawathira nkhondo popeza ankhondo awo anali osakonzekera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Gideoni anakwerera njira ya iwo okhala m'mahema kum'mawa kwa Noba, ndi Yogibea, nakantha khamulo popeza khamulo linakhala lokhazikika mtima.