Judges 8:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumeneko adagwira mnyamata wa ku Sukoti, nayamba kumfunsa mafunso. Mnyamatayo adalembera Gideoni maina a atsogoleri ndi a akuluakulu ena a ku Sukoti, okwanira makumi asanu ndi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anagwira mnyamata wa anthu a ku Sukoti, nafunsira; ndipo anamsimbira akalonga a ku Sukoti, ndi akulu ake amuna makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumeneko iye anagwira mnyamata wa ku Sukoti ndipo atamufunsa, mnyamatayo anamulembera mayina a akuluakulu ndi atsogoleri 77 a ku Sukoti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anagwira mnyamata wa anthu a ku Sukoti, nafunsira; ndipo anamsimbira akalonga a ku Sukoti, ndi akulu ace amuna makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi awiri.