Judges 8:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Gideoni adabwera kwa anthu a ku Sukoti naŵauza kuti, “Naŵa anthu aja, Zeba ndi Zalimuna, aja munkandinena nawoŵa kuti, ‘Kodi Zeba ndi Zalimuna waŵagonjetsa kale, m'mene ukuti tiŵapatse buledi anthu ako otopa kwambiriŵa?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Zalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Gideoni anabwera kwa anthu a ku Sukoti ndi kunena kuti, “Awa ndi Zeba ndi Zalimuna, mafumu awiri munkandinena nawo aja kuti, ‘Kodi Zeba ndi Zalimuna wawagonjetsa kale mmene ukuti tiwapatse buledi anthu ako otopawa?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Tsalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?