Judges 8:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Gideoni adafunsa Zeba ndi Zalimuna kuti, “Kodi anthu amene mudaŵapha ku Tabori aja ankaoneka bwanji?” Iwo adayankha kuti, “Aliyense ankaoneka monga momwe ukuwonekera iwemu. Ankaoneka ngati ana a mfumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anati kwa Zeba ndi Zalimuna, Amunawo munawapha ku Tabori anali otani? Iwo nayankha, Monga iwe momwemo iwowa; yense wakunga mwana wa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anafunsa Zeba ndi Zalimuna kuti, “Kodi anthu a ku Tabori amene munawapha aja anali a maonekedwe otani?” Iwo anayankha kuti, “Anali anthu a maonekedwe ngati inu. Aliyense ankaoneka ngati mwana wa mfumu?” Iwo anayankha kuti, “Anthu ngati inu, aliyense wooneka ngati mwana wa mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anati kwa Zeba ndi Tsalimuna, Amunawo munawapha ku Tabori anali otani? Iwo nayankha, Monga iwe momwemo iwowa; yense wakunga mwana wa mfumu.