Judges 8:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo adauza Yetere, mwana wake wachisamba, kuti, “Tiye, ipha anthuŵa.” Koma mnyamatayo sadasolole lupanga lake pakuti ankaopa, chifukwa anali akali mnyamata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati kwa Yetere mwana wake woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolole lupanga lake; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anawuza Yetero, mwana wake wachisamba kuti, “Tiye, ipha anthu amenewa!” Koma chifukwa Yeteri anali wamngʼono sanasolole lupanga lake, popeza anachita mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati kwa Yeteri mwana wace woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolola lupanga lace; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata.