Judges 8:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Zeba ndi Zalimuna adauza Gideoni kuti, “Mutiphe ndinu, pakuti inuyo ndiye muli ndi mphamvu za munthu wamkulu.” Pamenepo Gideoni adapha Zeba ndi Zalimuna. Ndipo adachotsa mphande zimene zinali m'khosi mwa ngamira zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Zeba ndi Zalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yake. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Zalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwa ngamira zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Zeba ndi Zalimuna anawuza Gideoni kuti, “Bwera utiphe ndiwe chifukwa uli ndi mphamvu za munthu wamkulu.” Choncho Gideoni anapita nawapha natenganso zokongoletsera zimene zinali pa makosi a ngamira zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Zeba ndi Tsalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yace. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Tsalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwa ngamila zao.