Judges 8:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kulemera kwake kwa ndolo zagolide zimene anthu adaperekazo kunali makilogramu 20, osaŵerengera kulemera kwa mphande, ukufu wam'khosi, zovala zofiira za mafumu a Midiyani, ndiponso malamba am'khosi a ngamira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kulemera kwake kwa maperere agolide adawapempha ndiko masekeli chikwi chimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zovala zachibakuwa za pa mafumu a ku Midiyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamira zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono kulemera kwa ndolo zagolide zimene anapereka kunali makilogalamu makumi awiri, osawerengera kulemera kwa mphande, mkanda wamʼkhosi, zovala zapepo za mafumu a Midiyani ndiponso malamba azitsulo za mʼmakosi a ngamira zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kulemera kwace kwa mapelele agolidi adawapempha ndiko masekeli cikwi cimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zobvala zacibakuwa za pa mafumu a ku Midyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamila zao.