Judges 8:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi golideyo adapanga efodi naikhazika mu mzinda wake ku Ofura. Tsono Aisraele onse adasiya Mulungu nayamba kupembedza efodiyo kumeneko, ndipo idasanduka msampha kwa Gideoniyo ndi kwa banja lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mudzi mwake, ndiwo Ofura; ndi Israele yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yake ngati msampha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gideoni anagwiritsa ntchito golide uja kupanga efodi, ndipo anakamuyika ku mzinda wake ku Ofura. Tsono Aisraeli onse anasiya kupembedza Yehova nayamba kupembedza efodiyo kumeneko. Ichi chinasanduka msampha kwa Gideoni ndi banja lake lonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mudzi mwace, ndiwo Ofira; ndi Israyeli yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yace ngati msampha.