Judges 8:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Amidiyani adagonjetsedwa ndi Aisraele ndipo sadayesenso zoŵaukira. Motero dziko lidakhala pa mtendere zaka makumi anai pa nthaŵi ya Gideoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero anagonjetsa Amidiyani pamaso pa ana a Israele, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m'masiku a Gideoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Amidiyani anagonjetsedwa ndi Aisraeli ndipo sanayeserenso kuwawukira. Ndipo dzikolo linakhala pa mtendere kwa zaka 40 pamene Gideoni anali ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero anagonjetsa Amidyani pamaso pa ana a Israyeli, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m'masiku a Gideoni.