Judges 8:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu wapereka m'manja mwanu mafumu a Midiyani, Orebu ndi Zebu. Ndachita chiyani kuyerekeza ndi zimene mwachita inu?” Gideoni atanena mau amenewo, anthuwo mitima yao idatsika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu anapereka m'dzanja lanu akalonga a Midiyani, Orebu ndi Zeebu, ndipo ndinakhoza kuchitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu wapereka mafumu a Midiyani, Orebu ndi Zeebu mʼmanja mwanu. Ndachita chiyani kuyerekeza ndi zimene mwachita inu?” Atanena izi, anthuwo mitima yawo inatsika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu anapereka m'dzanja lanu akalonga a Midyani, Orebi ndi Zeebi, ndipo ndinakhoza kucitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa.