Judges 8:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atafika ku mudzi wa Sukoti, Gideoni adapempha eni mudziwo kuti, “Chonde, apatseniko buledi anthu ali ndi ineŵa, pakuti atopa kwambiri. Tikupirikitsa Zeba ndi Zalimuna, mafumu a Midiyani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndilikulondola Zeba ndi Zalimuna mafumu a Midiyani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika ku Sukoti anapempha anthu a kumeneko kuti, “Chonde apatseniko buledi ankhondo angawa pakuti atopa. Koma ine ndikupirikitsa Zeba ndi Zalimuna, mafumu a Midiyani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndirikulondola Zeba ndi Tsalimuna mafumu a Midyani.